Popitiliza kufalitsa uthenga wokhudza kasamalidwe ka chilengedwe komanso kudziwitsa anthu kagwiritsidwe ntchito ka mphamvu ya m’bwezera, kudzera m’masewero a Mpira wamiyendo ndi wa Mtchembere mbaye, bungwe la Renew’N’Able Malawi (RENAMA) kudzera mu ntchito yotchedwa Green and Inclusive Energy tsopano yafika mu ndime ya matimu anayi sabata ino.
Sukulu za sekondale zisanu ndi zitatu ndi zomwe zakhala zikupikisana ndipo ma Sukulu anayi ndi omwe anachilimika kufika nawo mu ndine za Sukulu zinayi ku Lunzu ndinso Chileka m’mzinda wa Blantyre.
Sukulu zomwe zakwanitsa kufika nawo mu ndime ya matimu anayi ndi; St George yomwe inapalana mamba ndi Chigumukire ku Chileka, mu mpira wa miyendo ndi manja omwe. Pomwe Ngumbe inasasathana ndi Amazing Grace, mpira wa miyendo ndinso Amazing Grace inasasathana ndi Trinity pa masewero a Mtchembere mbaye ku Lunzu. Masewera a GIE akuchititsa ndi Chithandizo chochokera ku HIVOS kudzera ku Renew’N’Able Malawi (RENAMA).
Bambo Kenneth Mtag, omwe ndi Advocacy Officer wa RENAMA akusiyanitsa kwambiri pakati pa mpira wa sabata yatha ndi wasabata inu, poti sabata ino anthu anabwera mwa unyinji kusiyana ndi sabata yomwe Bonanza inayamba. A Mtago anawonjezeranso ponthirila mang’ombe kuti anthu ozawonera pamodzi ndi osewera amaonetsa chidwi.
“Masewera a lero ayenda bwino kwambiri poti tinaona matimu akubwera mu nthawi yabwino, komanso anthu anaonetsa chidwi pobwera kudzaonera, kudzamva uthenga omwe timafalitsa kuphatikiziranso kutenga nawo gawo popanga nawo mpikisano omwe amapambana ma T-shirt ndi zipewa” anatero a Mtago
Iwo anaonjezeranso ponena kuti, sakuyang’ana kulimbikitsa luso la a chinyamata lokha, komanso akufuna kuonetsetsa kuti chitukuko cha dziko lino chikuyenda bwino polimbikitsa anthu kugwiritsa ntchito zithu zogwilitsa ntchito mphamvu za m’bwezera. Iwo anati akukhutira ndi mmene akufalitsira uthenga wawo komanso akudalira anthu omwe anali pa malowa kupitiliza kuwadziwitsa anzawo omwe sanathe kufika pamalopa.
Potsiliza anati RENAMA ikuyembekezera kuti ndime yomaliza ikhala yapamwamba kwambiri, poti si ma timu ndi anthu okha omwe akapezeke pa malowa, komanso kukakhala mabungwe osiyanasiyana omwe amapanga zipangizo zogwilitsa ntchito mphamvu za m’bwezera akakhala akuonesa zipangizo zawo.
“Tikuyembekezera kuti kulimbirana ukatswiri kudzakhala kopambana pa lunzu, pamene pakakhale mwayi wa ma kampani ndi ma bungwe,omwe akugwira ntchito za m’bwezera ndi kuwaphunzitsa anthu mwa chimveveve kuti tikati mphamvu za m’bwezera ndi chani?, Nanga zikupindura bwanji? Ndinso tingazisamale bwanji?” anatero a Mtago
Pa masewero omwe anachitika pakati pa St George ndi Chigumukire kwa anyamata, St George inapambana ndi chigoli chimodzi kwa duu! (1-0), pomwe kwa atsikana St George inapambana ndi zigoli 27-17 Chigumukire, ku Chileka. Lunzu mpira wa atsikana Amazing Grace inapambana ndi zigoli 29-14 Trinity. Mpira wa anyamata, Ngumbe inapambambana ndi zigoli zitatu pomwe Amazing Grace inagoletsa zigoli ziwiri (3-2).
Izi zikusonyeza kuti St George izapikisana ndi Amazing Grace mpira wa Mchembere mbaye. Ngumbe izapikisana ndi St George Mpira wamiyendo pa ndime yotsiliza pa Lunzu primary school ground pa 9 November.